Phangano ya osewenzetsa

Phangano ya osewenzetsa

Phangano ya osewenzetsa ("Phangano")

Kothera pamene zinakonzedwapo: January, 24 2018.

Conde Werengani mosamala phangano ya osewenzetsa (“Phangano”) musanadinize pa batani ya “ndavomera”, musanatenge ndi kuika uthenga kapena kusewenzetsa BetBlocker ("Cosewenzera").

Podiniza batani ya "Ndavomera" Kutenga ndi kuika uthenga kapena kusewenzetsa Cosewenzera, ndiko kuti mwavomera kulondoza malamulo ya iyi Phangano.

Iyi Phangano ili pakati pa inu (inu nokha kapena bungwe limodzi) ndi a BetBlocker ndipo itsogolera masewenzedwe anu ya cosewenzera cimene a BetBlocker anakupatsani.

Ngati simuvomera malamulo amene ali mu phangano ili, osadiniza pa batani ya "ndavomera" ndipo osaika ndi kusewenzetsa cosewenzera.

Ici cosewenzera cinatetezedwa ndipo sicinagulitsidwe, kwa inu ndi a BetBlocker,kuti mucisewenzetse cabe kulingana ndi malamulo ali mu Phangano ili.


 

Chilolezo

A BetBlocker akupasani ufulu umene angatengenso, osafikapo, osapasa munthu wina, ufulu osafikapo kutenga ndi kusunga uthenga, kuika pa foni kapena pa kompyuta ndi kusewenzetsa mwekha, simuyenera kusewenzetsa ku zamalonda ai kulingana ndi lamulo la cosewenzera.



 

Kuteteza kasewenzetsedwe/zosabvomeresedwa

Muvomera kuti simudzacita ndipo simudzavomereza ena ku:

- kupasa ufulu wosewenzetsa, kugulitsa, kubwerekesa, kupasa. Kumwaza, kufalitsa, kusunga, kucotsa kwina, kuulula kapena kusewenzetsa cosewenzera kumalonda kapena kupasa ena cosewenzera.

- kukopera kapena kusewenzetsa cosewenzera mu njira ina yosavomerezedwa kulingana ndi ufulu mwapatsidwa pamwamba.

- kusintha, kupanganso nchito ina kucokera mu iyi, kuononga, kucotsapo zoletsa, kuononga cosewenzera conse kapena mbali imodzi monga mwamene anacipangira poyamba.

- kucotsa, kusintha kapena kubisa zili zonse za umwini (kuonjezerapo ufulu wa umwini ‘copyright’ kapena ‘trademark ‘) ya a BetBlocker kapena amene agwira nao nchito, opereka kapena amene apereka ufulu osewenzetsa cosewenzera.



 

Ufulu wa Umwini wosewenzetsa nzeru

Cosewenzera, kuonjezera ndi ufulu wa umwini monga copyright, patent, trademark, zamalonda za cisinsi, ndi ufulu osewenzetsa nzeru wina, ndipo zidzakhala, katundu wa a BetBlocker okha.


 

Maganizo anu

Mayankho anu, zokambapo, maganizo, zopititsa patsogoro (zonse pamodzi, “Maganizo”) mwapereka inu kwa BetBlocker zokhuzana cosewenzera zidzakhala katundu wa a BetBlocker okha.

A Betblocker adzakhala omasuka kusewenzetsa, kukopera, kusintha, kufalitsa kapena kugawanso maganizo munjira ina ili yonse kopanda kulesedwa kapena kukhala ndi nkhongole kapena kulipira inu.




 

Zosintha ku cosewenzera

A BetBlocker ali ndi ufulu osintha, kulekeza pa nthawi yocepa kapena kulekezerathu, cosewenzera kapena nchito ili yonse imene cosewenzera inalumikizana nazo kopanda kukuuzani ndipo kopanda kukhala ndi mulandu kwa inu.




 

Kukonza Cosewenzera

A BetBlocker adziika zopititsira patsogoro cosewenzera cao nthawi ndi nthawi, izi zingakhale zomendera, zocotsera tidoyo,zoikira patsogoro ndi zina ("Kukonza").

Kukonza kungapititse patsogolo mapangidwe ya cosewenzera kapena kufafaniza zina zosewenzetsa mu cosewenzera. Mwavomera kuti a BetBlocker (i) Sali ndi nchito yokukonzerani, kapena (ii) kupitiliza kukupatsani kapena kupanga zina zosewenzetsa ku cosewenzetsa canu.

Mupitilizabe kuvomera kuti kukonza konse (i) kudzakhala ndi nchito yaikulu ya cosewenzera, ndipo (ii) iyenera kucitidwa kulingana ndi malamulo ali mu phangano iyi.




 

Nchito Za Ena

Cosewenzera cingaonetse, kuonjezera kapena kuonetsa nchito za ena kapena zosewenzera zina (kuonjezera uthenga, zosewenzera ndi zinthu zina) kapena kupasa njira zolumikizira kwa ena kapena zosewenzera zina za ena.

Muzindikira ndi kuvomera kuti a BetBlocker sadzakhuzidwa ndi zinchito za ena, kuonjezera mu kasewenzedwe kao kazoona, kutherathu, kukhala ndi nthawi, uzoona, kukhala ndi lamulo ya umwini, kulondoza malamulo, ubwino, kapena mu njira ili yonse. A BetBlocker sadzakhuzidwa kwa inu kapena munthu wina ali yense kapena nchito za anthu ena.

Nchito za ena ndi njira zopezera ija nchito zipatsidwa cabe pothandiza ndipo kuti inu mupeze ndi kusewenzetsa. Pamene musewenzetsa, ziwani kuti simulandu wa a BetBlocker chifukwa muyeneya kulodoza malamulo ya aja ena anthu.





 

Kutenga nthawi ndi kutha kwa phangano

Iyi Phangano idzakhala ili kusewenza mpaka ikathetsedwe ndi a BetBlocker.

A BetBlocker mucifuniro cao okha, pa nthawi ili yonse ndipo pokhala chifukwa kapena popanda chifukwa, angaimitse kapena kuthetsa Phangano iyi atakudziwitsani kapena kopanda kukudziwitsani.

Iyi Phangano idzatha mosataya nthawi, kopanda kudziwitsidwa ndi a BetBlocker, ngati mwakangiwa kulondoza zili zonse zili mu Phangano iyi. Mungathetsenso Phangano iyi ngati mwacotsa cosewenzera ndi zina zace mufoni yano kapena mu kompyuta yanu.

Ngati Phangano iyi yatha, muyenera kuleka kusewenzetsa cosewenzera ca BetBlocker ndi kucicotsa mu foni kapena mu kompyuta yanu.





 

Kulipilidwa

Muvomera kusafuna kulipilidwa ndi a BetBlocker ndi cimake cao, tumakampani tocoka mu a BetBlocker, osewenza nao, anyanchito, othandizira pa nchito, ndi aja amene awapatsa ufulu ndi citupa cosewenza (ngati alipo) ngati kuli zoonongeka kapena zolipira zimene zingacoke cifukwa ca inu ku: (a) kasewenzetsedwe kanu ka cosewenzera; (b) kusalondoza Phangano iyi kapena lamulo ili yonse; Kapena (c) kusalondoza ufulu wa anthu ena.



 

Kulibe Lonjezo

Ici cosewenzera cipatsidwa kwa inu kulingana ndi mwamene cilili ndi zonse zosasewenza bwino kopanda lonjezo ili yonse. Kulingana ndi mwamene lamulo ivomerezera a BetBlocker, m’malo mwa iwo okha ndiponso m’malo mwa amene asewenza nao, ndi amene awapatsa ufulu ndi chitupa cosewenzera akukanirani poyera lonjezo lobweza, ngankhale kupitira mu lamulo kapena zina, kuona pa cosewenzera, kuonjezera malonjezo onse a zamalonda, kasewenzedwe ka cosewenzera, kukhala ndi chitupa ca umwini ndi zina za malonjezo zimene zingabwere pamene musewenzetsa, kasewenzetsedwe, kapena zamalonda. Kopanda cocotsapo pa izi zili pa mwamba, a BetBlocker sakulonjezani kuti cosewenzera cao sicingakupatseni bvuto ili yonse ndipo cingakhale ndi zonse zimene mufuna, mukwanilitsa kupeza zimene mufuna, zilowana bwino ndi zosewenzera zina kopanda bvuto, zisewenza bwino mu njira ili yonse, zodalilika, kulibe zobvuta kapena zobvuta zikapezeka zingakonzedwe.

Kopanda cocotsapo pa zili pa mwamba, a BetBlocker kapena amene asewenza nao salonjeza zili zonse pa cosewenzera cao (i) kasewenzedwe kapena zimene zilimo mu cosewenzera cao; (ii) kuti cosewenzera cao sicidzakupatsani bvuto; (iii) Kulonjeza ngati ndi cazoona ndipo codalilika; (iv) kuti cosewenzera cao, nchito cisewenza, kapena mauthenga apa mphepo otumidwa ndi a Betblocker kapena m’malo mwa a BetBlocker sicili ndi tidoyo kapena zili zonse zingaononge mafoni kapena ma kompyuta anu.

M'malo ena ufulu olonjeza kubweza sumapatsidwa kwa ogula, tero, zina kapena zonse zili pa mwamba sizingakukhuzeni.




 

Polekezera kutengako mbali

Kopanda kuona pa zoonongeka zimene mungakumane nazo, kumbali ya a BetBlocker ndi ofalitsa ao onse ali mu zimene zili mu Phangano iyi, ndi ufulu olipilidwa ngati mwapeza bvuto kufika cabe kulingana ndi ndalama zimene munalipira pamene munagula cosewenzera.

Kufika pamene lamulo ingavomereze, a BetBlocker ndi ofalitsa ao sadzakhuzidwa mu njira ili yonse pa zoonongeka zimene zingabwere mu njira ili yonse ( kuonjezerapo kusapeza ndalama za pamwamba, kusowetsa uthenga, kusokonezeka kwa malonda, kudzipweteka kwanu kapena zina zili zonse zobwera pamene musewenzetsa kapena kusasewenzetsa bwino cosewenzetsa ca Bet Blocker ndi ena osewenza nao, kapena mu njira ina ili yonse kulingana ndi Phangano), ngakhale kuti a BetBlocker kapena ofalitsa ao audzidwa pa bvuto ingabwere chifukwa ca izi kapena kulipilidwa kwakanga.

Maiko ena savomereza kuteteza zoonengeka zimene zingabwere kucoka mu izi, tero sizonse zili pa mwamba zingakhuze inu.





 

Kuononga kwa Phangano

Ngati mbali ili yonse mu Phangano iyi siili ndi mphamvu ya lamulo, mbaliyo iyenera kusinthidwa ndi kuitathauzira kuti ilondoze zolinga za mbali ya lamuloyo ndipo mbali zina za lamulo zidzakhalabe ndi mphamvu ndi kupitiliza kulondoledwa.




 

Kuika padera

Pokhapo ngati sicinalembedwe mu Phangano, kulephera kusewenzetsa ufulu kapena kuleka munthu wina kucita zoyenera kulingana ndi zili mu Phangano, sicidzateteza munthu kucoka kusewenzetsa ufulu, kapena kuleka munthu wina kucita zimene ayenera kucita pa nthawi ili yonse pambuyo kapena kuika padela kuonongeka kwa Phangano sicitanthauza kuti Phangano ngati yaonongeka idzaikidwanso pa mbali.




 

Kukonzedwanso kwa iyi Phangano

A BetBlocker ndi eni ace a ufulu, kulingana ndi mwamene afunira iwo okha, angasinthe Phangano pa nthawi ili yonse. Ngati mbali ina ya Phangano ndi yofunikira kusintha, tidzakupatsani masiku makhumi atatu (30 days) kuti mupitemo mu Phangano ya tsopano. Pazofunikira kusinthidwa ici cidzakhala cifuniro cathu.

Kupitiliza kusewenzetsa cosewenzera cathu pambuyo pa mbali zina kukhazikitsidwa, citanthauza kuti muvomera malamulo ya tsopano. Ngati simuvomera malamulo ya tsopano, simuloredwanso kusewenzetsa cosewenzera cathu.



 

Lamulo Imene Ilamulira

Lamulo yaku United Kingdom kucoserako malamulo ena oyangana pa zamkangano, ndiyo ilamulira kasewenzetsedwe kanu ka cosewenzera ndi Phangano iyi. Kasewenzetsedwe kanu ka cosewenzera kadzaonedwaponso ndi malamulo ena a dziko lonse ndi maiko ena.




 

Kuyamba Kusewenzetsa

Kuyamba kusewenzetsa cosewenzera ca BetBlocker citanthauza kuti mwavomera kuti mwawerenga ndi kumvesetsa kuti cosewenzera ici cidzakuletsani kusewenzetsa zosewenzera zina zokhuzana ndi zosewelera njuga yapa mphepo. Ndiponso muvomekezanso kuti cosewenzera sicidzacotsedwa pa kanthawi kovomerezedwa. Ndiponso mwavomeranso kuti anyanchito athu adzakuthandizani kucotsa tidoyo ta cosewenzera nthawi zonse pamene akwanitsa, koma sadzakuthandizani kucotsa cosewenzera.



 

Phangano Yonse

Phangano iyi ndi Phangano yonse ili pakati pa inu ndi a BetBlocker yokhuzana ndi kasewenzetsedwe ka cosewenzera ndipo ipitilila maphangano onse yanaliko kapena yali kupangidwa pamodzi ndi iyi, yolembedwa kapena yapakamwa.

Mungapatsidwe malamulo ena owonjenjerapo ngati musewenzetsa kapena kugula zosewenzera zina za BetBlocker, zimene a BetBlocker adzakupatsani pa nthawi yosewenzetsa kapena yogula.




 

Mwamene Mungakambire ndi Ife

Ngati muli ndi mafunso pa za iyi Phangano, conde tumani kusewenzetsa [email protected]